Talent wednesday
MPHATSO ZA MZIMU WOYERA
Wolemba: Innocent Masina Nkhonyo 30th July,2008
SENDERANI chifupi makosana ndi madona inu
Ndikupakulireni wa mzimu woyera mtakura
Ndiye atilengera maphata a wotenderedwa bwino maluso
kasupe wa za awoo zachikhakhali ntchedzero
mmisiri wa tsimba la wothyakuka bwino malangizo
Ngati wopota kabula
Wobwitimizidwa ndi Deneka wa khekhekhe
Ndiye atimangira mauvuni wowotchera zikondamoyo za matamando
Atilukira mathungwa mzimu woyera
Wotchezera chidulocha athu mayamiko kwa Mphambe Mulungu wa Mbona
Kudzera mu wombwandira chidwiwo athu maluso
Muyitaneni Phwendule
Thobwa la ulaliki adzatsope nawo mbamba
Ndinena wothethetsedwa mokankha mwazi uthenga
Ndi awo woyera kuda nakufuna a Juliano Kanyongolo
Poti nawo mchikhatho anawafumbatitsa yozunazunatu mphatso
Si inanso koma ija yofwanthamula loyera lemba
wisuwisu nkhope inali ndwii Nasuwandeyu
waphethira atasusa lake philikaniro
Mu msuzi wa mingoli ya magitala
Ndinena msambo zokwidzingwidwa ndi wathuyo mngelezi Paul Naluso
ummhu wa luso ati nanga wake mfunda
Athawatu kwa a Nebaku anawa
Zitawapeza zonyamula moyo ng’oma
Za ija yotsitsimutsa kwaya ndinena ya Chanco Catholic mboba inu
Poti nawonso ali nalo luso
Mbamba ya mzimu woyera mphatso anambwandira nawo
Jealous down nkhululu sasiya msuzi mtakuwuzani
Tilinayo ya maluso mitunga
Adatiwedzera mzimu woyera
Awo zachita tewa zifuwa ndi ija ya ndimanga khwekhwe nkhawa
Alikitimulireni uja wothambitsa msunamo gule
Poti yanu ija yotakasa chiuno mphatso
Adakuninkhanitu Yahweh, kuti osasanthidwa ndi nkhawa azanu
inu muwathuzitse chawo chimkankha mwazi
Awatu asiya zili gadaa m’mbale nthumbwana
Anyezi akuchita fulukutufulukutu mumsuzi wonyenzimira ngati kalilore
Nawo ati kudzafwanthamula sitepe
Litawambwandira chidwi la Yamikani liwu uko ku YCS
paja nayenso ali nalo lake luso
lofulula chitukwi cha mayimbidwe
[...] Read more
poem by Innocent Masina Nkhonyo
Added by Poetry Lover
Comment! | Vote! | Copy!
